Mavesi a m'Baibulo Onena za Chidziwitso
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Chidziwitso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa. “Pakuti mwakana kudziwa, Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga; chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu, Inenso ndidzayiwala ana anu.
ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.
Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo,
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso.
Munthu wanzeru amawonjezera nzeru zina; amafunafuna kudziwa bwino zinthu.