Mavesi a m'Baibulo Onena za Chifuniro cha Mulungu
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Chifuniro cha Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.
Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.
Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.
Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite.
Mulungu wamtendere, amene kudzera mʼmagazi a pangano lamuyaya anaukitsa Ambuye athu Yesu kwa akufa, amene ndi Mʼbusa wamkulu, akupatseni chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake ndipo Mulungu achite mwa ife, chimene chingamukomere kudzera mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ku nthawi zanthawi, Ameni.
Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama;
Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa.
Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba.
Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera.
Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa.
Phunzitseni kuchita chifuniro chanu, popeza ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.
“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.
Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha.
Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’