Mavesi a m'Baibulo Onena za Kumvetsetsa

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kumvetsetsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 3:13

Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

02 Miyambo 4:7

Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru. Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.

03 Miyambo 2:2-3

ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu; ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,

04 Masalimo 119:104

Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu; kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

05 Miyambo 3:5

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

06 Miyambo 16:16

Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.

07 Masalimo 119:130

Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika; ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.

08 Yobu 28:28

Ndipo Iye anati kwa munthu, ‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ”

09 Miyambo 9:10

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.

10 Miyambo 14:33

Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu, koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru.

11 1 Akorinto 14:20

Abale, lekani kuganiza ngati ana. Mukhale ana pa nkhani ya zoyipa koma mʼmaganizo anu mukhale okhwima.

12 Miyambo 18:2

Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu, koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.

13 Akolose 1:9

Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa.

14 Miyambo 19:8

Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake. Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.

Mitu yofanana