Mavesi a m'Baibulo Onena za Dalirani, Musatsamire
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Dalirani, Musatsamire oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
Pereka njira yako kwa Yehova; dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye. Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”
Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.
Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.
Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira munthu.
Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru, koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.