Mavesi a m'Baibulo Onena za Mawu Amakhalitsa Muyaya
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Mawu Amakhalitsa Muyaya oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
Pakuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka, koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.” Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Mawu anu Yehova ndi amuyaya; akhazikika kumwambako.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Ndinaphunzira kalekale kuchokera mʼmaumboni anu kuti maumboni amene munakhazikitsawo ndi amuyaya.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.
Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,” akutero Yehova.
Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri. Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.