Mavesi a m'Baibulo Onena za Malemba
Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Malemba oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo
Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.
Lamulo la Yehova ndi langwiro, kutsitsimutsa moyo. Maumboni a Yehova ndi odalirika, amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.
Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi.