Mavesi a m'Baibulo Onena za Mphamvu ya Mawu

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Mphamvu ya Mawu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Ahebri 4:12

Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.

02 Yesaya 55:11

Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.

03 Yeremiya 23:29

Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.

04 Aroma 1:16

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene.

05 1 Atesalonika 2:13

Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira.

06 Luka 1:37

Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”

07 Genesis 1:3

Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.

08 Yohane 6:63

Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.

Mitu yofanana