Mavesi a m'Baibulo Onena za Nyale ya Mapazi Anga

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Nyale ya Mapazi Anga oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 119:105

Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.

02 Masalimo 119:130

Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika; ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.

03 Miyambo 6:23

Paja malamulo awa ali ngati nyale, malangizowa ali ngati kuwunika, ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo moyo weniweni,

04 2 Petro 1:19

Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu.

05 Yohane 8:12

Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”

06 Masalimo 19:8

Malangizo a Yehova ndi olungama, amapereka chimwemwe mu mtima. Malamulo a Yehova ndi onyezimira, amapereka kuwala.

07 Masalimo 43:3

Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu kuti zinditsogolere; mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kumene inu mumakhala.

08 Miyambo 4:18

Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.

09 Masalimo 119:11

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

Mitu yofanana