Mavesi a m'Baibulo Onena za Kusunga Mawu Mumtima

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kusunga Mawu Mumtima oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 119:11

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

02 Deuteronomo 6:6-7

Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.

03 Akolose 3:16

Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.

04 Masalimo 119:9

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu.

05 Miyambo 7:1-3

Mwana wanga, mvera mawu anga; usunge bwino malamulo angawa. Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo; samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako. Uchite ngati wawamangirira pa zala zako, ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.

06 Deuteronomo 11:18

Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu.

Mitu yofanana