Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukhazikika pa Mawu
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kukhazikika pa Mawu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.” Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.
“Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe.
Mawu anu Yehova ndi amuyaya; akhazikika kumwambako.
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Mawu anu onse ndi owona; malamulo anu onse olungama ndi amuyaya.
Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,
Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.