Mavesi a m'Baibulo Onena za Kusinkhasinkha Mawu
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kusinkhasinkha Mawu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.
Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku. Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
Ndimalingalira malangizo anu ndipo ndimaganizira njira zanu.
Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu! Ndimalingaliramo tsiku lonse.
Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.
Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku, kuti ndithe kulingalira malonjezo anu.
Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
Ndimakumbukira masiku amakedzana; ndimalingalira za ntchito yanu yonse, ndimaganizira zimene manja anu anachita.
Ndidzakumbukira ntchito zanu ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”