Mavesi a m'Baibulo Onena za Munthu Sadzakhala ndi Moyo ndi Chakudya Chokha
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Munthu Sadzakhala ndi Moyo ndi Chakudya Chokha oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”
Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.
Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ ”
Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake; ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.
Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”
Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.
Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino. Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala. Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndimadziwika ndi dzina lanu.
Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha.
“Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse; osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi, koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,
Yesu anati, “Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake.
“Bwerani, dzadyeni chakudya changa ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa, otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!