Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Amene Amaona

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Mulungu Amene Amaona oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Genesis 16:13

Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: “Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, “Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.”

02 Miyambo 15:3

Maso a Yehova ali ponseponse, amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.

03 Masalimo 139:1-2

Inu Yehova, mwandisanthula ndipo mukundidziwa. Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka; mumazindikira maganizo anga muli kutali.

04 Ahebri 4:13

Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.

05 2 Mbiri 16:9

Pakuti Yehova amayangʼana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi kuti alimbikitse iwo amene mitima yawo ayipereka kwathunthu kwa Iye. Inu mwachita chinthu chopusa ndipo kuyambira lero mudzakhala pa nkhondo.”

06 Masalimo 33:13-15

Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi ndi kuona anthu onse; kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira onse amene amakhala pa dziko lapansi. Iye amene amapanga mitima ya onse, amaona zonse zimene akuchita.

07 Yeremiya 23:24

Kodi wina angathe kubisala Ine osamuona?” “Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?” Akutero Yehova.

08 Masalimo 139:7-10

Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu? Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu? Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko; ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko. Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa, ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja, kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.

09 Yobu 34:21

“Maso a Mulungu amapenya njira za munthu; amaona mayendedwe ake onse.

10 Masalimo 11:4

Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.

11 Miyambo 5:21

Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona, ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.

12 Masalimo 121:3-4

Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera. Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona.

13 Luka 12:6-7

Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu. Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.

Mitu yofanana