Mavesi a m'Baibulo Onena za Wamphamvuzonse

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Wamphamvuzonse oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Chivumbulutso 1:8

“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”

02 Genesis 17:1

Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse.

03 Chivumbulutso 4:8

Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti, “Woyera, woyera, woyera ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.”

04 Masalimo 91:1

Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.

05 Yobu 42:2

“Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse; chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.

06 Yeremiya 32:17

“Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani.

07 Genesis 1:1

Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

08 Yesaya 40:28

Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Yehova ndiye Mulungu wamuyaya, ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi. Iye sadzatopa kapena kufowoka ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.

09 Mateyu 19:26

Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”

10 Masalimo 147:5

Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri; nzeru zake zilibe malire.

11 Chivumbulutso 15:3

Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati, “Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona, Mfumu ya mitundu yonse.

Mitu yofanana