Mavesi a m'Baibulo Onena za Thanthwe

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Thanthwe oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 18:2

Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo. Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.

02 Deuteronomo 32:4

Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa, Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.

03 Masalimo 62:2

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.

04 1 Samueli 2:2

“Palibe wina woyera ngati Yehova, palibe wina koma inu nokha, palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.

05 Masalimo 18:31

Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?

06 2 Samueli 22:2-3

Iye anati, “Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga. Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

07 Yesaya 26:4

Mudalireni Yehova mpaka muyaya, chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.

Mitu yofanana