Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Ndi Kuwala
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Mulungu Ndi Kuwala oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.
Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”
Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndi linga la moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Kuwunika kunawala mu mdima, koma mdimawo sunakuzindikire.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.
Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo; mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.
Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire, kapena mwezi kuti uwunikire usiku, pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya, ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.
Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika; amadziwa zimene zili mu mdima, ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.
Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja.