Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Ndi Chikondi

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Mulungu Ndi Chikondi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Yohane 4:8

Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.

02 1 Yohane 4:16

Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.

03 1 Yohane 4:19

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda.

04 Yohane 3:16

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

05 Aroma 5:8

Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.

06 1 Yohane 4:9

Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo.

07 Yeremiya 31:3

Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati, “Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire. Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.

Mitu yofanana