Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Wamuyaya

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Mulungu Wamuyaya oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Deuteronomo 33:27

Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’

02 Masalimo 90:2

Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

03 Yesaya 40:28

Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Yehova ndiye Mulungu wamuyaya, ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi. Iye sadzatopa kapena kufowoka ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.

04 Chivumbulutso 1:8

“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”

05 1 Timoteyo 1:17

Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

06 Masalimo 102:25-27

Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu. Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo; zidzatha ngati chovala. Mudzazisintha ngati chovala ndipo zidzatayidwa. Koma Inu simusintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.

07 Habakuku 1:12

Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire? Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa. Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo; Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.

08 Yesaya 57:15

Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

09 2 Petro 3:8

Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi!

10 Masalimo 93:2

Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale; Inu ndinu wamuyaya.

11 Ahebri 13:8

Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse.

Mitu yofanana