Mavesi a m'Baibulo Onena za Chifundo kwa Ena
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Chifundo kwa Ena oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Odala ndi amene ali ndi chifundo, chifukwa adzawachitira chifundo.
Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.”
chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.
Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira. Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu.
Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni.
Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.
Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.
Kodi iwe sukanamuchitira chifundo wantchito mnzako monga momwe ine ndinakuchitira iwe?’
Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe, ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
Muwachitire chifundo amene akukayika.