Mavesi a m'Baibulo Onena za Khalani M'mawu
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Khalani M'mawu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga.
Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa.
ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.
Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.
Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
Onetsetsani kuti zimene munazimva kuyambira pachiyambi zikhalebe mwa inu. Ngati zikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndiponso mwa Atate.
Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.
Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi.
Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi.
Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera.
Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye.
Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa ntchito zako. Taona, ndakutsekulira pa khomo ndipo palibe wina amene angatseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa komabe wasunga mawu anga ndipo sunandikane.