Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuchitira Umboni

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Kuchitira Umboni oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Ife sitingaleke kuyankhula za zimene tinaziona ndi kuzimva.”

03 1 Petro 3:15

Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.

04 Yohane 15:27

Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”

05 Mateyu 5:16

Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.

06 Aroma 10:9-10

kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.

07 Yohane 1:46

Natanieli anafunsa kuti, “Nazareti! Kodi kanthu kalikonse kabwino kangachokere kumeneko?” Filipo anati, “Bwera udzaone.”

Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva.

09 Masalimo 66:16

Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.

10 Yohane 9:25

Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!”

11 Marko 5:19

Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.”

Mitu yofanana