Mavesi a m'Baibulo Onena za Mapazi Okongola

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Mapazi Okongola oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 10:15

Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”

02 Yesaya 52:7

Ngokongoladi mapazi a amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri. Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere, chisangalalo ndi chipulumutso. Iwo akubwera kudzawuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wako ndi mfumu!”

03 Aroma 10:14

Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo?

04 Nahumu 1:15

Taonani, pa phiripo, mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, amene akulengeza za mtendere! Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu ndipo kwaniritsani malumbiro anu. Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; iwo adzawonongedwa kotheratu.

Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

06 Aroma 10:13

pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”

07 1 Akorinto 9:16

Komatu ndikamalalikira Uthenga Wabwino, sindingadzitamandire popeza ndimawumirizidwa kulalikira. Tsoka kwa ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino!

08 2 Akorinto 5:20

Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

09 Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.

Mitu yofanana