Mavesi a m'Baibulo Onena za Mitundu ya Anthu

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Mitundu ya Anthu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 96:3

Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

02 Masalimo 67:1-2

Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire. Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

03 Yesaya 49:6

Yehovayo tsono akuti, “Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobo ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka. Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira, udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”

04 Mateyu 28:19

Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,

05 Habakuku 2:14

Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga momwe madzi amadzazira nyanja.

06 Masalimo 22:27

Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye, ndipo mabanja a mitundu ya anthu adzawerama pamaso pake,

07 Chivumbulutso 7:9

Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.

08 Genesis 12:3

Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe, ndi kutemberera amene adzatemberera iwe; ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.”

09 Masalimo 86:9

Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye; iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.

10 Yesaya 2:2

Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse, lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.

Mitu yofanana