Mavesi a m'Baibulo Onena za Zokolola

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Zokolola oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 9:37-38

Pamenepo anati kwa ophunzira ake, “Zokolola ndi zambiri koma antchito ndi ochepa. Nʼchifukwa chake, pemphani Ambuye mwini zokolola kuti atumize antchito ku munda wake.”

02 Yohane 4:35

Kodi inu simunena kuti, ‘Kwatsala miyezi inayi ndipo kenaka kukolola?’ Ine ndikukuwuzani kuti, tsekulani maso anu ndipo muyangʼane mʼminda! Mbewu zacha kale kuti zikololedwe.

03 Luka 10:2

Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola.

04 Agalatiya 6:9

Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.

05 Masalimo 126:5-6

Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe. Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.

06 Yohane 4:36

Ngakhale tsopano amene akukolola akulandira malipiro ake, ndipo akututa mbewu ku moyo wosatha kuti wofesa ndi wokolola asangalale pamodzi.

07 Mateyu 13:30

Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ ”

08 Marko 4:29

Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”

Tsono mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana”

10 Yakobo 5:7

Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza.

11 Hoseya 10:12

Mufese nokha chilungamo ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika. Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo; pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova, mpaka Iye atabwera kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.

12 2 Akorinto 9:6

Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.

Mitu yofanana