Mavesi a m'Baibulo Onena za Fuko Lililonse ndi Lilime Lililonse

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Fuko Lililonse ndi Lilime Lililonse oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Chivumbulutso 7:9

Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.

02 Chivumbulutso 5:9

Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti, “Inu ndinu woyenera kulandira bukuli ndi kumatula zomatira zake, chifukwa munaphedwa, ndipo magazi anu munagulira Mulungu anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.

03 Masalimo 22:27

Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye, ndipo mabanja a mitundu ya anthu adzawerama pamaso pake,

04 Afilipi 2:10-11

kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko, ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.

05 Danieli 7:14

Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.

06 Chivumbulutso 5:13

Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti, “Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa, kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya!”

07 Yesaya 45:23

Ndalumbira ndekha, pakamwa panga patulutsa mawu owona, mawu amene sadzasinthika konse akuti, bondo lililonse lidzagwada pamaso panga; anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.

08 Aroma 14:11

Kwalembedwa, akutero Ambuye, “Pamene Ine ndili ndi moyo, aliyense adzandigwadira ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.”

09 Zekariya 8:23

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”

Mitu yofanana