Mavesi a m'Baibulo Onena za Pitani Mukauze
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Pitani Mukauze oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.”
Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse, ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.
Kenaka mayiyo anasiya mtsuko wamadzi, nabwerera ku mzinda ndipo anati kwa anthu, “Tiyeni mukaone munthu amene wandiwuza ine zilizonse zimene ndinazichita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu?”
Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?” Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”
Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”
Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse.
Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu.
Mngeloyo anati, “Pitani, ku mabwalo a Nyumba ya Mulungu ndipo mukawuze anthu uthenga onse wamoyo watsopanowu.”
Choncho chimene Andreya anachita ndi kukapeza mʼbale wake Simoni ndipo anamuwuza kuti, “Ife tamupeza Mesiya,” (kutanthauza kuti Khristu).
Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.