Mavesi a m'Baibulo Onena za Kayankhulidwe Kabwino
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kayankhulidwe Kabwino oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.
Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve.
Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo, koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.
Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga zikhale zokondweretsa pamaso panu, Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.
Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.
Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo, koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.
Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu. Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri; koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.
Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.
Ana anjoka inu, woyipa inu, mungathe bwanji kuyankhula kanthu kalikonse kabwino? Pakuti pakamwa pamayankhula zosefuka kuchokera mu mtima. Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye.
Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru, ndipo mawu ake amawonjezera nzeru.
Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika.
Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera, ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.
Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi.
Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.