Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudalitsa Ena
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kudalitsa Ena oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere.
Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso.
Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani.
“ ‘Yehova akudalitse ndi kukusunga; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitira chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.’ ”
Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani
“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.