Mavesi a m'Baibulo Onena za Miseche

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Miseche oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 16:28

Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano, ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri.

02 Miyambo 11:13

Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi; koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.

03 Miyambo 20:19

Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi. Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.

04 Miyambo 26:20

Pakasowa nkhuni, moto umazima; chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.

05 Levitiko 19:16

“ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu. “ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.

06 Miyambo 18:8

Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma; amalowa mʼmimba mwa munthu.

Mitu yofanana