Mavesi a m'Baibulo Onena za Mawu Olimbikitsa

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Mawu Olimbikitsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 4:29

Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve.

02 Miyambo 12:25

Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu, koma mawu abwino amamusangalatsa.

03 1 Atesalonika 5:11

Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.

04 Ahebri 3:13

Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.

05 Miyambo 16:24

Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

06 Miyambo 25:11

Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.

07 Yesaya 50:4

Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka. Mmawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.

08 Akolose 4:6

Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.

09 Miyambo 15:23

Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera, ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.

Mitu yofanana