Mavesi a m'Baibulo Onena za Kunena Choonadi
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Kunena Choonadi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Mʼmalo mwake, poyankhula choonadi mwachikondi, tidzakula mu zinthu zonse ndi kukhala thupi la Khristu, amene ndi Mutu, omwe ndi mpingo.
Zinthu zoti muchite ndi izi: Muziwuzana zoona zokhazokha, muziweruza moona ndi mwachilungamo mʼmabwalo anu;
Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi.
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
Mawu woona amakhala mpaka muyaya koma mawu abodza sakhalitsa.
Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake
asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.
Pakuti, “Iye amene angakonde moyo ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake kuyankhula zoyipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.
Pakamwa panga pamayankhula zoona ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.