Mavesi a m'Baibulo Onena za Mbewu ya Mawu

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Mbewu ya Mawu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Luka 8:11

“Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu.

02 Luka 8:15

Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.

03 Marko 4:20

Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”

04 1 Petro 1:23

Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

05 Mateyu 13:23

Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”

06 Marko 4:14

Wofesa amafesa mawu.

07 Luka 8:8

Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.” Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.”

08 Mateyu 13:3-9

Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa. Amene ali ndi makutu amve.”

09 Yakobo 1:21

Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.

10 Yesaya 55:10-11

Monga mvula ndi chisanu chowundana zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko koma zimathirira dziko lapansi. Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya. Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.

11 Marko 4:26-27

Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira.

12 1 Akorinto 3:6

Ine ndinadzala mbewu, Apolo anayithirira, koma Mulungu ndiye anayikulitsa.

13 Luka 8:5

“Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya.

14 Yohane 12:24

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’

15 Agalatiya 6:7-8

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

Mitu yofanana