Mavesi a m'Baibulo Onena za Nsembe ya Matamando
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Nsembe ya Matamando oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake.
Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza, ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse chipulumutso cha Mulungu.”
Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere.
Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe ndikuyimba nyimbo yamayamiko. Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa. Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”
Kotero mutu wanga udzakwezedwa kuposa adani anga amene andizungulira; pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe; ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.
Apereke nsembe yachiyamiko ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu; ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova, pakuti ndi labwino.
Bweretsani zopempha zanu ndipo bwererani kwa Yehova. Munene kwa Iye kuti, “Tikhululukireni machimo athu onse ndi kutilandira mokoma mtima, kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.