Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyimbira Mulungu

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kuyimbira Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 96:1

Imbirani Yehova nyimbo yatsopano; Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.

02 Masalimo 98:1

Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa; dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zamuchitira chipulumutso.

03 Aefeso 5:19

Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu.

04 Masalimo 100:2

Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.

05 Akolose 3:16

Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.

06 Masalimo 95:1

Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe, tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu

07 Masalimo 147:7

Imbirani Yehova ndi mayamiko; imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.

08 Masalimo 33:3

Muyimbireni nyimbo yatsopano; imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.

09 Masalimo 104:33

Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse; ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.

Mitu yofanana