Mavesi a m'Baibulo Onena za Tamandani Yehova
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Tamandani Yehova oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga; ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
Ndidzayamika Yehova nthawi zonse; matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu.
Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga; ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi. Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
Tamandani Yehova, ntchito yake yonse kulikonse mu ulamuliro wake. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.
ndi ife amene timatamanda Yehova, kuyambira tsopano mpaka muyaya. Tamandani Yehova.
Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova, amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova.