Mavesi a m'Baibulo Onena za Kulambira

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kulambira oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 4:24

Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”

02 Masalimo 29:2

Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake, pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

03 Aroma 12:1

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.

04 Chivumbulutso 4:11

“Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”

05 Masalimo 100:2

Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.

06 Masalimo 95:6

Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;

07 Masalimo 96:9

Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake; njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.

08 Ahebri 12:28

Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha.

09 Eksodo 34:14

Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje.

10 Masalimo 99:5

Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mulambireni pa mapazi ake; Iye ndi woyera.

Mitu yofanana