Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyamika

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kuyamika oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 100:4

Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.

02 Masalimo 95:2

Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.

03 Masalimo 118:1

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

04 Aefeso 5:20

Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

05 2 Akorinto 9:15

Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!

06 Masalimo 136:1

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

07 1 Atesalonika 5:18

Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

08 Masalimo 107:1

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.

09 Akolose 3:17

Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

10 Afilipi 4:6

Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.

Mitu yofanana