Mavesi a m'Baibulo Onena za Ulemu
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Ulemu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha.
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye.
Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa: uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wa anthu onse.
Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.
Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.
Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera, ndiye amene uyenera kumuopa, ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
“ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.
Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.
Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri; Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.
Popeza mumapemphera kwa Atate amene amaweruza munthu aliyense mopanda tsankho molingana ndi zochita zake, pa nthawi imene muli alendo pa dziko lapansi khalani moopa Mulungu.