Mavesi a m'Baibulo Onena za Mkhalapakati
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Mkhalapakati oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.
Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija.
Kwa Yesu mʼkhalapakati wa pangano latsopano, ndiponso mwafika ku magazi owazidwa amene amayankhula mawu abwino kuposa magazi a Abele.
Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo.
Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi.
Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.