Mavesi a m'Baibulo Onena za Mbusa Wamkulu
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Mbusa Wamkulu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Mulungu wamtendere, amene kudzera mʼmagazi a pangano lamuyaya anaukitsa Ambuye athu Yesu kwa akufa, amene ndi Mʼbusa wamkulu,
Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.
Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.
“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
“Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa,
Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa: Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo.