Mavesi a m'Baibulo Onena za Womtchinjiriza Wathu
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Womtchinjiriza Wathu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo.
Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera.
Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.
Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.
Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu, adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza anapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe. Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri, ndipo anawapempherera anthu olakwa.
Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe. Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu.
Koma Yesu popeza ndi wamuyaya, unsembe wake ndi wosatha. Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.
Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye. Yehova anawuza Satana kuti, “Yehova akukudzudzula iwe Satana! Yehova amene wasankha Yerusalemu akukudzudzula! Kodi munthu uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”
Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha? Ndi Mulungu amene amalungamitsa. Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera.
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi.
Kwa Yesu mʼkhalapakati wa pangano latsopano, ndiponso mwafika ku magazi owazidwa amene amayankhula mawu abwino kuposa magazi a Abele.
Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba; wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.