Mavesi a m'Baibulo Onena za Mfumu ya Mafumu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Mfumu ya Mafumu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili: MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.

02 1 Timoteyo 6:15

Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye.

Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”

04 Masalimo 24:7-8

Tukulani mitu yanu inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe. Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.

05 Danieli 7:14

Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.

Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”

07 Masalimo 47:7-8

Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando. Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.

08 1 Timoteyo 1:17

Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

09 Zekariya 9:9

Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni! Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu! Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yolungama ndi yogonjetsa adani, yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu, pa mwana wamphongo wa bulu.

10 Masalimo 2:6

“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.”

11 Yesaya 9:6-7

Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere. Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.

Mitu yofanana