Mavesi a m'Baibulo Onena za Dzina la Yesu

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Dzina la Yesu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”

02 Afilipi 2:10-11

kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko, ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.

03 Mateyu 1:21

Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”

04 Yohane 14:13-14

Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.

Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.

06 Afilipi 2:9

Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri, ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse

07 Akolose 3:17

Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

08 Miyambo 18:10

Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.

09 Yohane 20:31

Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.

tsono dziwani izi inu ndi aliyense mu Israeli: munthuyu akuyima pamaso panu, wochiritsidwa kwathunthu, ndi chifukwa cha dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti amene munamupachika koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa.

11 1 Akorinto 6:11

Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.

12 Mateyu 18:20

Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”

13 Aroma 10:13

pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”

14 Yohane 16:23-24

Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

Ndipo aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’

Mitu yofanana