Mavesi a m'Baibulo Onena za Mbusa Wabwino
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Mbusa Wabwino oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.
Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
“Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa,
Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine. Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.
“ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima.
Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino, amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.
monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu.
Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa: Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.
“Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe
Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake.