Mavesi a m'Baibulo Onena za Ufumu wa Khristu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Ufumu wa Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Afilipi 2:9-11

Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri, ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko, ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.

02 Aroma 10:9

kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.

03 Akolose 1:16-17

Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye.

“Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”

05 1 Akorinto 12:3

Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.

06 Aefeso 1:20-22

imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba. Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo. Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo,

07 Mateyu 28:18

Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.

Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili: MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.

09 1 Akorinto 8:6

koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.

10 Yohane 13:13

Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili.

11 1 Petro 3:15

Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.

Mitu yofanana