Mavesi a m'Baibulo Onena za Yehova Mchiritsi Wathu

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Yehova Mchiritsi Wathu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Eksodo 15:26

Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”

02 Masalimo 103:2-3

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse. Amene amakhululuka machimo ako onse ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,

03 Yesaya 53:5

Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.

04 Yeremiya 17:14

Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira; pulumutseni ndipo ndidzapulumuka, chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.

05 Masalimo 147:3

Akutsogolera anthu osweka mtima ndi kumanga mabala awo.

06 Yeremiya 30:17

Ndidzachiza matenda anu ndi kupoletsa zilonda zanu, akutero Yehova, ‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika. Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”

07 Masalimo 30:2

Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.

08 Malaki 4:2

Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.

09 Mateyu 11:28

“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

10 1 Petro 2:24

Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.

11 Masalimo 41:3

Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.

12 Hoseya 6:1

“Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova. Iye watikhadzula, koma adzatichiritsa. Iye wativulaza, koma adzamanga mabala athu.

13 Luka 4:18

“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,

14 Masalimo 107:20

Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa; anawalanditsa ku manda.

15 Yakobo 5:14-15

Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.

Mitu yofanana