Mavesi a m'Baibulo Onena za Wamng'ono Koposa Mwa Awa
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Wamng'ono Koposa Mwa Awa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’
Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira, ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’
Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.
Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa.
Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”
“Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’
Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.
Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”
Ndipo Iye anawawuza kuti, “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”
“Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’
Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.
Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa?
Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu?
“Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.”