Mavesi a m'Baibulo Onena za Ulemerero wa Dzina Lake

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Ulemerero wa Dzina Lake oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 29:2

Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake, pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

02 Masalimo 8:1

Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba.

03 Afilipi 2:9-10

Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri, ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,

04 Masalimo 113:3

Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake, dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.

05 Malaki 1:11

Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

06 Masalimo 96:8

Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake; bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.

07 Yesaya 12:4

Tsiku limenelo mudzati: “Yamikani Yehova, tamandani dzina lake; mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.

08 Masalimo 72:19

Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. Ameni ndi Ameni.

Mitu yofanana