Mavesi a m'Baibulo Onena za Yankhulirani Osatha Kudziyankhulira

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Yankhulirani Osatha Kudziyankhulira oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 31:8-9

Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera. Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.

02 Yesaya 1:17

phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”

03 Masalimo 82:3-4

Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

04 Yeremiya 22:3

Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano.

05 Miyambo 24:11-12

Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe; uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa. Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?

06 Yobu 29:12

chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo, ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.

07 Masalimo 41:1

Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.

08 Estere 4:14

Pakuti ngati ukhalatu chete nthawi ino, chithandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina nʼkutheka kuti iwe ndi a pa banja la makolo ako mudzafa. Ndipo adziwa ndani mwina unalowa ufumu chifukwa cha nthawi ngati imeneyi?”

09 Miyambo 29:7

Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi.

Mitu yofanana