Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikhulupiriro Chopulumutsa

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Chikhulupiriro Chopulumutsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 2:8

Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu,

02 Aroma 10:17

Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

03 Ahebri 11:1

Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu.

04 Aroma 5:1

Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

05 Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

06 Yohane 3:16

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

07 Yohane 1:12

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;

08 Marko 16:16

Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.

Iwo anayankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako.”

10 Yakobo 2:17

Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

11 Ahebri 11:6

Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

Mitu yofanana